Rabies Education in Malawi: Gift’s Story

Post by
emily king
on
April 26th 2018

Our education work in Malawi is vital to ensuring we have as much impact as possible in the fight against rabies. By empowering children and community groups with the knowledge to protect themselves against this deadly disease, we are helping reduce human and canine deaths from rabies.

Our Malawi team have recently celebrated an incredible milestone – over 1,000,000 children educated about rabies!! Gift was just one child who has benefitted from these lifesaving lessons…

 

 

When Gift was bitten by a suspected rabid dog while walking home from school, he knew exactly what to do. He and his classmates had received a talk from a Mission Rabies’ education team, so he knew he had to wash the wound for 15 minutes using soap and water. He then made the long journey to the clinic where he received his post-exposure vaccinations. This journey was hundreds of kilometres and he travelled mostly on foot, but he and his family knew the vaccinations were critical for Gift’s survival.

 

Other members of Gift’s community still held tattered copies of the leaflets they had been given by Mission Rabies education teams the year before, so when two more people were bitten by the same dog shortly afterwards, they were also able to receive correct treatment following the information on the leaflets. Even Gift’s neighbour’s dog who was bitten was protected by his rabies vaccination given by Mission Rabies the previous year, and rather than being killed from fear of this disease, this community knew the dog was safe and could be kept in quarantine to ensure he received treatment.

 

We are so pleased to see the communities of Malawi responding well to the messages delivered by our teams and helping to spread the rabies prevention messages. These lessons are so important to ensure children like Gift are protected, and making sure families know how to act should a suspected rabies incident occur. Without these education lessons, Gift could have become just another of the child deaths that rabies still results in each year.

 

Together, we are working to eliminate rabies in Malawi and other world hotspots for the disease. Don't forget to keep up to date with the team's current work in Malawi as our Blantyre campaign is underway using our live page!

_ _ _

 

MAPHUNZIRO A CHIWEWE KU MALAWI: NKHANI YA GIFT

Ntchito yathu yophunzitsa ku Malawi ndiyothandiza kuthana ndi nthenda ya Chiwewe.Polimbikitsa ana komanso anthu a mmidzi kuti akhare odziwa momwe angazitetezere ku nthenda yomwe imaphayi, tikuthandiza kuchepetsa imfa zodza kamba ka nthendayi.

Anyamata athu omwe amaphunzitsa ndiokondwa pofikira ana 1million amene aphunzitsidwa zokhudzana ndi Chiwewe.Gift ndi mwana mmodzi yemwe wapindura ndi maphunzirowa.

Pamene Gift amabwera kuchokera ku sukulu analumidwa ndi galu yemwe amamuganizira kuti ndiwa Chiwewe.iye anadziwiratu zoyenera kuchita pakuti Gift ndi mzake analandirako maphunziro a Mission Rabies kuchokera kwa anyamata athu, nde anazindikira kuti akuyenera kutsuka pabala ndi sopo kwa mphindi khumi ndi zisanu pogwiritsa ntchito madzi. Atatha izi Gift ananyamuka ulendo opita ku Chipatala komwe anakalandira katemera. Ulendowu unali wamtunda wautali pafupifupi makilomita zana limodzi ndipo anayenda wapansi, iye pamodzi ndi banja lawo lomwe amafuna katemerayu.

Anthu ena okhara mdera lomwe Gift amachokera anali ndi mapepara omwe analandira kuchokera ku bungwe la Mission Rabies lophunzitsa mma sukulu Chaka chathacho. Anthu ena awiri omwe analumidwanso ndi galu yemweyi analandiranso chithandizo cholondora chomwe anawerenga mu timapepara tomwe analandirato. Ngakhare galu yemwe anayandikana ndi kwa Gift atalumidwa ndi galu wachiwewe anali otetezedwa kamba ka katemera yemwe anabaidwa ndi gulu la Mission chaka chatha,kusiyana kupha kamba koopa matendawa, anthuwa amadziwa kuti galu wawo ndi otetezedwa choncho kunali kwabwino kumuika kwarantaini kuti azilandira chithandizo.

Tili okondwa poona mizinda yaku Malawi momwe anthu akuyankhira mauthenga athu omwe akuperekedwa ndi anyamata athu okamba za momwe angazitetezere ku chiwewe. Maphunzirowa ndi othandiza kwa ana monga Gift komanso kuonetsetsa kuti mabanja akutha kudziwa zomwe angapange nthawi yomwe wina walumidwa ndi galu. Kupanda maphunziro amenewa Gift akanakhara mmodzi mwa ana omwalira kamba ka nthendayi yomwe ikuphabe anthu chaka chilichonse.

Tonse pamodzi tikugwira ntchito yolimbana ndikuthana ndi nthenda ya Chiwewe Mmalawi komanso maiko ena okhudzidwa ndi nthendayi.